Saturday, October 1, 2011

Nkhani za luso

Kuyambira lero, ndadzikhuthula ndekha pamaso panu Amalawi kuti ndidzilemba nkhani zosiyanasiyana zokhudza luso la makono. Kusiyana kwa chibaluwa ichi ndi zina zomwe zilipo kale ndi koti, padzikhala nkhani zambiri zolembedwa mChicheŵa koma zokamba za luso la makono. Ganizo limeneli laza chifukwa chakusowa kwa zibaluwa kapenanso madabwe amene amalemba zokhudza lusoli mchiyankhulo chathuchi. Inde poti mwachaje satafuna, pena ndidzitha kusakaniza tinantina poopa kuti maso angachite dalazi.

Ndidziyesetsa kulemba kawirikawiri kuti inu mudzikhala ndi choŵerenga mChicheŵa pa utatavupa. Ndikudziwanso kuti ena mudzivutika kuŵerenga mawu ena olembedwa mchibaluwachi. Choncho ndikonza mtanthauziramawu umene udzikhala ndi mawu amziyankhulo ziwiri, Chicheŵa ndi Chingerezi. Poyambirira pano, mtanthauziramawuwu ukhala pa Google Docs koma kenako, Ambuye akalola, ndiyesa kutsegula dambwe lakelake kuti mudzidzatha kufufuza mosavuta. Kwa iwo amene samadziwa, Google Docs ndi mphasha wa tizitakataka wa pa utatavu wa ulere wopangidwa ndi Google. Mawu ena amene adzigwiritsidwa ntchito pano, mutha kuwasakatulanso pa http://www.chichewadictionary.org/, mtanthauziramawu wolembedwa ndi ng'anga ya ukachenjede, a Steven Paas. 

Komanso ndifotokoze bwino lomwe kuti chifukwa pakali pano Chicheŵa chilibe mawu ambiri okhudza luso la makono, mawu ena ambiri omwe mudziwapeza pano ndi opolongeza ndekha. Ndiye ndikalakwitsa kagwiritsidwe ntchito ka mawuwo, chonde nditumizireni kakalata koserewula pa keyala izi: kachaleedmond [pa] gmail [dontho] com kapenanso chichewalocaliser [pa] gmail [dontho] com (ndazifwafwaza keyalazi poopa amalengankhuvi. Inu polembapo, mudzatsinthe [pa] kukhala @ ndinso [dontho] kukhala mpumiro ".", opanda mitengeroyi komanso mipata pakati pa mawuwo.)

Ndikukhulupirira kuti mudzisangalala nazo nkhani zomwe ndidzilemba pano. Mbambadi, Chicheŵa ndi cholama ndi mawu osiyanasiyana, ena oti inenso sindimawadziwabe mpaka lero. Tsono, ndiyesa kuti pano pakhala pa kachere potsitsira nthanthi ndi msinjiro zina za chiyankhulochi zokamba za luso la makono. Ngatinso ena muli nazo nkhani zoti nkugawana, ndiuzeni ndidzayesesa kuziyikapo.

1 comment: