Saturday, October 15, 2011

Kuyidziwa Kompsuta

Ambirife tinayiwonapo, tiyimadziwa ndipo timagwriritsa ntchito kompsuta. Ena mwina timangowamva mawuwa koma sitimamvetseta kuti ndi makina wotani, nanga amagwira bwanji ntchito. Penanso mwina timasokonezeka tikamva za utatavu, omwe ena amawutcha makina a intaneti. Kodi zinthu zimenezi zimasiyana bwanji? Nanga nzotheka kugwirirtsa ntchito kompsuta popanda utatavu? Kapenanso nzothekanso kodi kugwiritsa ntchito utatavu popanda kompsuta? Lero komanso masabata angapo ali nkudzawa, tikhala tikuunikirana zokhudza kompsuta ndi utatavu ncholinga choti tonse tizimvetsetse zinthu zimenezi. Ndikukhulupirira kuti tikhala limodzi poti kandimverere anakanena za mmaluwa.

Kompsuta ndi makina omwe anapangidwa mwaukadaulo oti adzichita kuwerengera ndi kuganiza mozama. Munthu amatha kuyituma kompsuta kuchita zinthu zina ndi zina monga kuwerengera ndalama, kutanthauzira zotsatira za kalembera wa dziko, kulosera nyengo ndi nthawi, kuyendetsera ndege, mwinanso kutsekera ndi kutsekulira nyumba kapena galula.

Makina a kompsuta amenewa mukanthawi kochepa amakwanitsa kuchita zinthu zoti mwina ife bwenzi zikutitengera miyezi ngakhalenso zakazaka tisanamalize, pena chifukwa kulakwitsa ndiye umunthuwo, mwina bwenzi tikungoleka kuti basi zatikanika. Makinawa anapangidwa mwaukachenjede kuti adzitha kutipepuza pochita zinthu. Ndikukhulupirira kuti inu amene mukuwerenga nkhani iyi muli pa kompsuta, ngati ayi ndiye kuti munatsindikiza nkhaniyi pa chikalata kugwiritsa ntchito kompsuta yomweyo.
Ziwalo za Kompsuta (wojambula woyamba: Micro Computer Center)

Makina a kompsuta amenewa ali ndi ziwalo zosiyanasiyana zoti sitingazitchule zonse pano. Koma kompsuta yonse inagawika pawiri ― zikwa ndi ulembo. Zikwa ndi ziwalo zonse za kompsuta zomwe ndi zokhudzika ndi manja. Ulembo ndi ndondomeko ya madongosolo yomwe imalamulira chilinchose zikwa zimachita. Kusiyana ndi zikwa, ulembo suukhudzika ndi manja athuwa. Tikhonza kungoona tizithunzi totilozera mitundu ya ulembo imene ili mu kompsuta mwathu, koma si ulembo uliwonse umene uli ndi tiakalozera timeneti. 

Zikwa zilipo mitundu angapo: chiphenipheni, kachesa, bawo la malembo ndi mlozo. Pa makompsuta ena pamathanso kukhala chinkuzamawu, mikwezamawu ndi makina wotsindikizira zikalata. Ulembo unagawidwa patatu: mwinimudzi, makako ndi madongoloso.

Chiphenipheni chimaoneka ngati kanema. Pamenepa ndi pomwe timaonera zinthu zosiyanasiyana zimene zili mu kompsuta yathu. 

Kachesa ndi amene amakhala ndi ubongo wa kompsuta. Mmenemo mukhala likanda la tizitakataka tathu tonse, dembedza komanso chibaza. Likanda limasunga mabuku athu, nyimbo, makanema komanso upangiri wa madongosolo a kompsuta yathu. Dembedza ndi ubongo wa kompsutayo. Kompsuta imagwiritsa ntchito dembedza pofuna kuchita chiganizo china chilichonse. Chibaza monga mwa dzina lake ndi chida chimene kompsuta imagwiritsa ntchito pofuna tsekula madongosolo ndikusungiramo tinthu koma mwa kanthawi. Zibaza zimachita kusomekedwa. Mukhodza kuchotsamo nkuyika zibaza zosiyana mmakulidwe. Mukhodzanso kuonjezera malingana ngati muli zisomeka zokwanira. Mukatsekula kachesa wa kompsuta, chibaza chimaoneka ngati mtima wa wayilesi.

Bawo la malembo ndi chinthu chomwe chili ndi mabutawo amene timagwiritsa ntchito pofuna kulemba kanthu komanso kuyituma kanthu kompsuta. Kompsuta zosiyanasiyana zimakhala ndi bawo za malembo zosiyanasiyananso. Koma kompsuta zambiri zimakhala ndi mabawo amene ali ndi mabutawo a manambala, a malembo, a chithandizo komanso ena otumira mauthenga ku ulembo wa kompsutazo. Bawo zinanso zimakhala ndi mabutawo owonjezera monga osewerera nyimbo komanso ochitira ntcherupe pa utatavu.

Mlozo ndi kachida kakang'ono kamene timagwiritsa ntchito pofuna kuloza, kusankha, kutosa kapena kutsegulira zinthu pa kompsuta. Ena amakatchula kuti mbewa pokasipa chifukwa cha dzina lake la mChingerezi. Milozo ilipo ya nthambo komanso ina yopanda nthambo. Milozo ya nthambo imalimikizidwa ku kompsuta pamene yopanda nthambo imagwira ntchito mwachinunu. Milozo ina imakhala ndi kampira koma yambiri ya makono ili ndi getsi pansi pawo. Mlozo umagwira ntchito powusisititsa pansi posamalika bwino poti usalowe madzi kapena fumbi. Ukamasisita pansipo, mlozowo umayendetsa namlondola pa kompsuta motsatira mmene inu mukuwuyendetseranso. Mlozo umakhalanso ndi mabutawo omwe mukhodza kuthabwanya pofuna kusankhira kapena kutsekulira kanthu pa kompsuta.

Mwinimudzi ndi ulembo umene umalamulira kompsuta yonse kuchita zinthu. Chilichonse chikafuna kuchitika mu kompsuta, monga kutsindikiza chikalata kapena kutsekula dongosolo, chimayamba chapempha chilolezo kwa mwinimudzi. Mwinimudzi ndi amene amadziwa ngati pali malo okwanira mchibaza oti nkuchitirapo kanthu komanso amayang'ana ngati dembedza alibe thangwanikwa zoti nkulepheretsa kuchita ntchito zina zoonjezera. Ulembo wa mwinimudzi uli ngati mzimu, suuoneka koma umagwira ntchito yotamandika ndipo popanda iwo, ndiye kuti kompsuta siingapange kalikonse.

Makako ndi gulu ulembo umene umachita zinthu zosiyanasiyana pa okha pofuna kuti kompsuta igwire bwino ntchito. Mwa chitsanzo, makako amafufuza nkhuvi zomwe zikudwalitsa kompsuta yathu. Ulembo umenewu umathanso kufufuza madongosolo amene ali owonjezera ku madogosolo omwe alipo kale kuti adzigwira bwino ntchito. Makako amagwira ntchito kwambiri mothandizana ndi mwinimudzi. Chifukwa cha ichi, makako ambiri saoneka. Amagwira ntchito ngati mizimu. Pali makako ena omwe amangopereka uthenga akaona kuti pali chofunika munthu adziwe kapena achite, monga kupalitsa kompsuta pa nyesi za magetsi pamene batile latha mphamvu kapenanso kuchenjeza za kugwedezeka kwa chitetezo cha kompsuta chifukwa chosowa katemera woyiteteza ku nkhuvi.

Dongosolo ndi ndondomeko imene anthu amagwiritsa ntchito pochita chinthu pa kompsuta. Zina mwa ndondomeko zimenezi ndi zosewerera nyimbo ndi makanema, zolembera kalata kapenanso zosewerera masewero pa kompsuta. Bawo ya Sekulu, gumbagumba ya Windows Media Player, kalembera wa Microsoft Word ndi zina mwa zitsanzo za madongosolo a pa kompsuta.

E!E! Zikachuluka sizidyeka. Bwanji kwa lero tilekane pamenepa. Sabata ya mawa tidzapitirize kusanthula zina nzina. Ndapita!!

Ngati muli ndi ndemanga pena mafunso mukhodza kulemba pa gawo la ndemanga pansipa kapenanso kunditumizira kalata yoserewula pa keyala izi:
kachaleedmond [pa] gmail [dontho] com kapenanso chichewalocaliser [pa] gmail [dontho] com
Chidziwitso: ndazifwafwaza keyalazi poopa amalengankhuvi. Inu polembapo, mudzatsinthe [pa] kukhala @ ndinso [dontho] kukhala mpumiro ".", opanda mitengeroyi komanso mipata pakati pa mawuwo.

No comments:

Post a Comment